546

 

MAPATA ATATU

Zindikira akumvere chisoni iwe Mulungu kuti ndithu nkofunika kwa ife kudziwa zinthu zinayi;

CHOYAMBA.

Kuzindikira kumudziwa Mulungu ndikumudziwa Mtumiki wake ndikudziwa chipembezo cha chisilamu ndi ma umboni ake.

CHACHIWIRI.

Kugwiritsa ntchito zimene mwazidziwazo.

CHACHITATU.

Kuwayitanira anthu kuzimene mwazidziwazo.

CHACHINAYI.

Kupirira ndi zowawa zimene ungakumane nazo pakuyitanirapo.

Umboni wake ndi mau a Mulungu onena kuti;

بسم الله الرحمن الرحيم

"والعصر إن الإنسان لفي خسر إلا الذ ين آمنوا وعملوا الصالحات وتواصوابالحق وتوا صوا باالصبر"

(سورة العصر:الآيات 1-3)

MDZINA LA MULUNGU WACHIFUNDO CHAMBIRI WACHISONI.

  1. Ndikulumbirira nthawi.
  2. Ndithu munthu aliyense ndi wotayika{chifukwa chakugonjetsedwa ndi zilakolako zake}
  3. Kupatula amene akhulupirira {mwa Mulungu} ndikumachita zabwino, ndikumalangizana kusatira choona ndiponso ndikumalangizana zakupirira {potsatira malamulo a Mulungu ndi zina zovuta za mdziko}.

      [Surat Asir: Ayat 1-3]

Akunena Imamu Shaffie {amumvere chisoni Mulungu} kuti; "Kukanakhala kuti sanatsitse Mulungu umboni pa zolengedwa zake nkungotsitsa Surat iyi yokha basi ikanakwanira."

Ndipo Imamu Bukhari amumvere chisoni Mulungu akuti;" Khomo lonena zakuzindikira kusanayambe kulankhula komanso kugwira ntchito,

Umboni wake Mulungu akuti;

فاعلم أنه لا إله إلا هو واستغفر لذنبك

(سورة محمد: الآية 19)

Mulungu wayamba kutchula zakuzindikira kusanayambe kulankhula komanso kugwira ntchito.

"Dziwa kuti palibe wompembedza m`choonadi koma Mulungu ndipo pempha chikhululuko pazolakwa zako."

[Surat Muhammad Ayat: 19]

Dziwa akumvere chisoni iwe Mulungu kuti; ndikofunika kwa msilamu aliyense wam`muna ndi wamkazi kuzindikira zinthu zitatu {izi} ndikuzigwiritsa ntchito.

CHOYAMBA.

Ndithu Mulungu watilenga ndipo akutipatsa chakudya, ndiye sanangotisiyanso choncho koma watitumizira ife mtumiki, tsono munthu amene atsatire Iye akalowa ku Mtendere {Jannat} ndipo amene anyoze mtumiki akalowa ku chilango cha moto.

Umboni wa mawu amenewa Mulungu akuti;

إنا أرسلنا إليكم رسولاً شاهدا عليكم كما أرسلنا إلى فرعون رسولاً. فعصى فرعون الرسول فأخذناه أخذاً وبيلاً. (سورة المزمل:الآيتان 15-16)

"Ndithu Ife takutumizirani mthenga amene adzakhala mboni yanu{tsiku la chimaliziro} monga momwe tidamtumizira {Musa} kukhala mtumiki kwa Firiauni. Koma Firiauni adamunyoza mtumikiyo ndipo tidamulanga chilango chokhwima.

[Surat Muzammil:Ayat 15-16]

CHACHIWIRI.

Ndithu Mulungu samasangalala kuti aphatikizidwe pamodzi ndi Iye mu mapemphero ake ndi aliyense angakhale m`ngelo amene ali kufupi ndi Iye kapenanso mtumiki amene wotumidwa.

Umboni wake Mulungu akuti;

"وأن المساجد لله فلا تدعوا مع الله أحداً.

(سورة الجن الآية 18)

"Ndithu mizikiti ndi ya Mulungu yekha! Choncho, musapembedze aliyense pamodzi ndi Mulungu."

[Surat Jinni Ayat: 18]

CHACHITATU.

Ndithu munthu amene akutsatira mtumiki komanso akukhulupirira umodzi wa Mulungu, sikololedwa kwa iye kukonda anthu amene akumuda Mulungu ndi mthenga wake, angakhale akhale ofupikitsitsa pokhala pawo.

Umboni wake Mulungu akuti;

"لا تجد قوماً يؤمنون بالله واليوم الآخر يوادون من حاد الله ورسوله ولو كانوا آباءهم أو أبناءهم أوإخوانهم أو عشيرتهم أولئك كتب في قلوبهم الإيمان وأيدهم بروح منه ويدخلهم جنات تجري من تحتها الأنهار خالدين فيها رضي الله عنهم ورضوا عنه أولئك حزب الله ألا إن حزب الله هم المفلحون."

{سورة المجادلة الآية 22}

"Supeza anthu okhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza akukonda amene akumuda Mulungu ndi mthenga wake ngakhale atakhala atate awo, ana awo, abale awo, ndi akuntundu wawo, kwa iwo{Mulungu} wazika chikhulupiriro {champhamvu} m`mitima mwawo ndipo wawalimbitsa ndi mphamvu zochokera kwa Iye. Ndipo adzawalowetsa m`minda yomwe pansi pake pakuyenda mitsinje, adzakhala m`menemo muyaya. Mulungu adzakondwera nawo ndipo {iwonso} adzakondwera naye. Iwowa ndi chipani cha Mulungu. Dziwani kuti chipani cha Mulungu ndi chopambana."

[Surat Mujadalat Ayat: 22]

Dziwa akuwongole iwe Mulungu potsatira Iye kuti chipembedzo choyera cha Ibrahim ndiko kuti ugwadire ndikupempha Mulungu m`modzi moyeretsa chipembedzo chake. Choncho, adalamula Mulungu anthu onse ndiponso adawalenga ndi chifukwa chimenechi monga m`mene akunenera Mulunguyo;

"وما خلقت الجن والإنس إلا ليعبدون."

{سورة الذاريات الآية 56}

"Sindidalenge ziwanda {Majini} ndi anthu koma kuti azindipembedza."

[Surat Dhariat Ayat: 56]

Kumasulira liwu lotiيعبدون}} Azindipanga kukhala Ine wandekha. Komanso chachikulu chimene adalamula Mulungu ndi TAUHID; uko ndiko kumuyika Mulungu kukhala wayekha mu mapepmphero ake. Chachikulu chomwe Mulungu waletsa ndi SHIRIKI; kumeneko ndiko kupempha mophatikiza Iye ndi china.

Umboni wake Mulungu akuti;

"واعبدوا الله ولا تشركوا به شيئاً."

{سورة النساء الآية 36}

"Ndipo mpembedzeni Mulungu ndipo musamphatikize ndi chiri chonse."

[Surat Nisai Ayat: 36]

Ngati ungafunsidwe kuti; kodi mapata atatu amene akufunika kwa munthu kuwadziwa ndi ati?

Nena:

Kudziwa kapolo mbuye wake ndi chipembedzo chake, ndi mtumiki wake Muhammad {SAW}.

Ngati ungafunsidwe kuti; kodi Mbuye wako ndi ndani?

Nena:

Mbuye wanga ndi Mulungu amene wandilera ine komanso walera zolengedwa zonse ndi mtendere wake, Iye ndi womulambira wanga ndiribe wina womulambira woposa Iye.

Umboni wake Mulungu akuti;

"الحمد لله رب العالمين."

{سورة الفاتحة الآية 2}

"Kutamandidwa konse nkwa Mulungu Mbuye wazolengedwa zonse."

[Surat Fatiha Ayat: 2]

Chiri chonse chimene chisali Mulungu ndicholengedwa ndipo ine ndi m`modzi wa zolengedwa zimenezi.

Ngati ungafunsidwe kuti; Wamudziwa ndi chani bwana wako?

Nena kuti:

Ndizisonyezo zake komanso ndi zolengedwa zake.  Zina mwazisonyezozi ndi monga usiku ndi usana, dzuwa ndi mwezi. Zina mwazolengedwa zake ndi monga Mitambo isanu ndi iwiri [7] ndi madothinso asanu ndi awiri [7] komanso ndi zinthu zimene ziri mkati mwazimenezi ndinso zimene ziri pakati pake.

Umboni wake Mulungu akuti;

"ومن آياته اليل والنهار والشمس والقمر لا تسجدوا للشمس ولا للقمر واسجدوا لله الذي خلقهن إن كنتم إياه تعبدون."

{سورة فصلت الآية 37}

"Ndipo zina mwazisonyezo zake, ndi usiku ndi usana, dzuwa ndi mwezi. Musalambire dzuwa ngakhale mwezi, koma lambirani Mulungu {m`modzi} amene adazilenga ngati inu mumpembedza moona."

[Surat Fuswilat Ayat: 37]

 

Komanso mawu a Mulungu;

"إن ربكم الله الذي خلق السماوات والأرض في ستة أيام ثم استوى على العرش يغشي اليل والنهار يطلبه حثيثاً والشمس والقمر والنجوم مسخرات بأمره ألا له الملك تبارك الله رب العالمينز"

{سورة الأعراف الآية 54}

"Ndithudi Mbuye wanu ndi Mulungu yemwe adalenga thambo ndi nthaka m`masiku asanu ndi limodzi. Kenako adakhazikika pa mpando wake wachifumu. Amauchita usiku kuti uvindikire usana zimatsatana mwamsangamsanga. Ndipo dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi nzofewetsetsa {zikuyenda mogonjera} ndi Lamulo Lake. Dziwani kuti kulenga nkwake ndiponso kulamula nkwake. Ndithudi watukuka Mulungu mbuye wazolengedwa zonse."

[Surat Araf Ayat 54]

Mbuye Iye ndi wolambiridwa.

Umboni wake Mulungu akuti;

"ياأيها الناس أعبدوا ربكم الذي خلقكم والذين من قبلكم لعلكم تتقون. الذي خلق لكم الأرض فراشاً والسماء بناءً وأنزل من السماء ماءً فأخرج به من الثمرات رزقاً لكم فلا تجعلوا لله أنداداً أنتم تعلمون."

{سورة البقرة الآية 21-22}

"E! Inu anthu! Pembedzani Mbuye wanu yemwe adakulengani inu ndi omwe adalipo kale kuti, muzitchinjirize {kuchilango cha Mulungu {Mulungu} yemwe adakupangirani nthaka kukhala ngati mphasa ndi thambo kukhala ngati denga, ndipo adatsitsa madzi kuchokera ku mitambo natulutsa ndi madziwo zipatso zosiyanasiyana kuti chikhale chakudya chanu. Choncho Mulungu musampangire anzake uku inu

Mukudziwa {kuti alibe wothandizana naye}.

[Surat Baqara Ayat: 21-23]

Ibn Kathir   Akunena kuti:

{Amene walenga izi zonse ndiye oyenera kumpembedza}

Mitundu ya Ibada [Mapempheero} imene Mulungu walamula ndi monga chisilamu ,

Chikhulupiliro ndi ubwino.

Zina mwa zimenezo ndi Duwa { kupempha} kuopa, kufuna, kuyadzamira, khumbo, mantha, kudzichepetsa, kutembenuka , kupempha chithandizo, kupempha chitchinjirizo, kuzinga ,lonjezo ndi zina zotero muzinthu zomwe Mulungu adalamulira.

Umboni ndi mau a Mulungu amene akuti   

(وأن المساجد لله فلا تدعوا مع الله أحدا) الجن 18

Ndithu mizikiti ndi ya Mulungu yekha, choncho musapembedze aliyense pamodzi ndi Mulungu.

{Surat Jinni: Ayat 18}

Munthu amene atembenuze chimodzi mwa zinthu zimene zachitidwandikupangira osakhala Mulungu {m’modzi} iye ndi mushiriki, ophatikiza Mulungu ndi zina m’mapemphero komanso iye ndi Kafiri. {Okanira chilungamo cha Mulungu}.

 

Umboni wake Mulungu akuti:

قال تعالى: (ومن يدع مع الله إلاها ءاخرلا برهان له به فإنما حسابه عند ربه إنه لا يفلح الكافرون)

سورة المؤمنون: اية 117

Ndipo amene apembedze Mulungu wina pophatikiza ndi Mulungu {weniweni} chikhalirecho iye alibe umboni pa zimenezo basi chiwelengero chake chili kwa mbuye wake. Ndithu osakhulupilira sangapambane.

{Surat Muuminina: Ayat 117}

Mtumiki Muhammad {SAW} akunena mu hadith yake kuti:

( الدعاء مخ العبادة)

Duwa (Kupempha) ndi bongo wa Mapemphero.

Umboni wake Mulungu akuti:

قال تعالى   :  (  وقال ربكم أدعونى أ ستجب لكم إن الذين يستكبرون عن عبادتي سيد خلون جهنم داخرين )

سورة غافر:اية 60           

Ndipo Mbuye wanu wanena kuti: (ndipempheni ndikuyankhani koma amene akudzikweza ndi mapemphero anga (posiya kundipembedza), adzalowa ku Jahanama ali oyaluka).

(Surat Ghafiri: Ayat 60).

Umboni wa kuopa, Mulungu wanena kuti:

قال تعالى: (فلا تخافوهم وخافون ان كنتم مؤمنين)

(سورة آل عمران:الآية 175)

Choncho musawaope,  ndiopeni Ine ngati inu muli okhulupirira.

(Surat Al Imran: Ayat 175)

Umboni wakufuna; Mulungu akuti:

قال تعالى:(فمن كان ير جو لقاء ربه فليعمل عملا صالحا ولا يشرك بعبادة ربه أحدا)

                    ( سورة الكهف الآية 110)                             

(Ndipo amene afuna kukumana ndi mbuye wake, achite zochita za bwino ndipo asaphathikize aliyense pa mapemphero ambuye wake)

Surat Al kahafi: Ayat 110.

Umboni wa kuyadzamira, Mulungu akunena kuti:

قال تعالى:  ( وعلى الله فتوكلوا إن كنتم مؤمنين)   سورة المائدة: الأية 23               

Ndipo  kwa Mulungu yekha yadzamilaningati inu mulidi okhulupilira.

{ Surat  Almaida,Ayat 23}

mulungu akunenanso kuti,

قال تعالى: ( ومن يتوكل على الله فهو حسبه سورة الطلاق الأية 3           

Ndipo amene akutsamira kwa Mulungu {pa zinthu zake zonse} ndiye kuti Mulungu ali okwana kwa iye kumkozera chilichonse.  [Surat Atwalaq Ayat 3}

Umboni wakhumbo, mantha ndikudzichepetsa, Mulungu akuti;

( إنهم كانوا يسارعون في الخيرات ويدعوننا رغبا ورهبا وكانوا لنا خاشعين سورة الأنبياء الأية 9    

 

Ndithu iwo adali achangu pochita zabwino, ankatipempha mwa khumbo ndi mwa manthandipo adli odzichepetsa kwa Ife.

{Surat Al-anmbiya Ayat 90}

Umboni wakuopa Mulungu akuti,

قال تعالى: (فلا تخشوهم واخشونىسورة البقرة  الأية 150    

Umboni wa kutembenuka Mulungu akuti,

قال تعالى:( وأنيبوا الى ربكم فأسلموا له) سورة الزمر الأية 54     

Ndipo tembenukirani kwa mbuye wanu ndipo m’gonjereni.

[Surat Zumara Ayat 54]

Umboni wa kupempha chithandizo Mulungu akuti,

قال تعالى: ( إياك نعبد وإياك نستعين) سورة الفاتحة الأية 5     

Inu nokha tikupembedzani ndiponso inu nokha tikupemphani chithandizo.

{Surat Alfatih Ayat 5}

Mtumiki Muhammad {S.A.W} mu Hadith yake akuti,

( إذا استعنت فاستعن باالله )   

Ukapempha chithandizo, udzipempha kwa Mulungu  

Umboni wa kudzitchinjiriza Mulungu akuti,

قال تعالى: ( قل أعوذ برب الناس ملك الناس ) سورة الناس  الأيتان 1-2  

Nena: ndikudzitchinjiriza ndi Mbuye [Mleri] wa anthu {yemwe akulinganiza zinthu zawo}. Mfumu ya anthu Imene ili ndi mphamvu yochita chilichonse pa iwo.

[Surat Anas Ayat 1-2]

 

 

 

Umboni wa kupempha chithandizo, Mulungu akuti:

قال تعالى: ( إذ تستغيثون ربكم فاستجاب لكم ) سورة الأنفال الأية 9  

Kumbukirani panene mudali kupempha  Mbuye wanu chithandizo, ndipo anakuyankhani.

[Surat Anfal: Ayat 9]

Umboni wa kuzinga Mulungu akunena kuti:

قال تعالى : ( قل إن صلاتي ونسكي ومحيا ى ومماتي  لله رب العالمين. لا شريك له وبذلك امرت وأنا أول المسلمين ).

سورة  الأنعام الأية  162- 163 

Nena ndithudi, swala yanga mapemphero anga onse, moyo wanga ndi imfa yanga zonse ndi za Mulungu. Mbuyw wa zolengedwa zonse.iye alibe othandizana naye. Izi ndi zomwe ndalamulidwa ndipo ine ndi oyamba mwa ogonjera.

[Surat Anfal Aayat 162-163]

Mtumiki Muhammad [S.A.W.] akuti:

قال رسول الله صلى الله عليه وسلم : ( لعن الله من ذبح لغير الله

Watembelera Mulungu munthu amene wazinga posakhala mwa Mulungu.

Umboni woti munthu akwanilitse lonjezo Mulungu akuti:

قال تعالى: ( يوفون بالنذر ويخافون يوما كان شره مستطيرا )

 سورة  الإنسان الأية  7

Amene akukwanilitsa zimene adalonjeza kwa Mulungu ndiponso akuopa tsiku lalikulu limene zoipa zake zidzakhala zofalikira ponseponse.

[Surat Insani: Ayat 7]

 

 

PHATA LACHIWIRI:   KUDZIWA CHIPEMBEDZO CHA CHISILAMU NDI MAUMBONI AKE.

Kodi chisilamu ndi chiyani?

Chisilamu ndi kudzipeleka mwa Mulungu pomupanga Iye kukhala wayekha m’mapemphero Ake ndi kutsogozedwa ndi Iye pomutsatila malamulo Ake, ndikupewa kumuphatikiza, ndikupewanso zina za mtundu umenewu.

Ndipo Chipembedzochi chili m’magawo atatu awa:

1-Chisilamu

2-Chikhulupiliro

3-Ubwino 

Gawo lililonse lili ndi nsichi zake ndipo nsichi za chisilamu zilipo zisanu.

 Nsichi yoyamba.

Kupangira umboni kuti palibe wina oyenera kumugwadira muchoonadi koma Mulungu m’modzi ndipo ndithu Muhammad ndi mthenga wake.

Nsichi yachiwiri

Kuimika swala. [Mapemphero]

Nsichi ya chitatu

Kupeleka chopeleka [Zaka]

Nsichi ya chinayi

Kusala mwezi wa Ramadhan.

Nsichi ya chisanu.

Kupita ku nyumba ya Mulungu yolemekezeka kukapanga mapemphero a Hajj.

Mau a Mulungu akunena za kuchitila umboni, Mulungu akuti:

قال تعالى: ( شهد الله أنه لا إلاه  إلا هو والملائكة وأولو العلم قائما با لقسط لا إ لاه إلا هو العزيز الحكيم )

سزرة العمران : الأية  18           

Mulungu [mwini] akuikila umboni kuti, palibe wopembedzedwa muchoonadi koma iye basi ndipo akuikila umboni [zomwe] Angelo ndi eni nzeru kuti iye ngokhazikitsa chilungamo. Palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma iye. Ngwamphamvu zoposa, ngwa nzeru za kuya.  {Surat Alimran: Ayat 18}

Mauwa akumasulira kuti: palibe wina oyenera kulambiridwa muchoonadi koma Mulungu yekha.  

Kukana zonse zimene zimalambilidwa kusiya Mulungu. Ndiponso kutsimikizira kuti mapemhpero onse omupangira wake ndi Mulngu yekha basi, iye alibe osakanikilana naye mumapemmphero monganso iye alibe othandizana naye mu ufumu wake.

Kumasulira kwa mauwa ndi komveka kuchokera mukunena kwa Mulungu.

قال تعالى: ( وإذ قال إبراهيم لأبيه وقومه إننى براء مما تعبدون إلا الذى فطرني فإنه يهدين وجعلها كلمة باقية فى عقبه لعلهم يرجعون )

سورة الزخرف الآيات 26- 28        

Ndipo kumbuka pamena Ibrahim adawuza bambo ake ndi anthu ake kuti, ndithu ine ndidzipatula kuzimene mukuzipembedzazi kupatula amene adandilenga ndithu iye andiongola. Ndipo adachita liu ili kukhala losatha ku mtundu wake, kuti abwelere {kumalankhulidwe amenewa}.

[Surat Azukhruf Ayat 26-28]

Maunso a Mulungu akuti:

قال تعالى: ( قل ياأهل الكتاب تعالوا إلى كلمة سواء بيننا وبينكم ألا تعبدوا إلا الله ولا تشرك به شيئا ولا يتخذ بعضنا بعضا أربابا من دون الله فإن تولوا فقولوا اشهدوا بأنا مسلمون )

سورة آل عمران الأية  64)  )

Nena; " Inu eni Buku la Mulungu [Ayuda ndi Akhristu] Idzani ku liu lolingana pakati pathu ndi Inu {lakuti} tisapembedze aliyense koma Mulungu mmodzi yekha ndiponso tisamphatikize ndi chiri chonse ena mwa Ife asawasandutse anzawo kukhala milungu m`malo mwa Mulungu." Ngati atembenuka ndikunyoza nenani; "Ikirani umboni kuti Ife ndife asilamu {ogonjera malamulo a Mulungu}".

[Surat Al-Imran Ayat: 64

Mau a Mulungu akunena za kuchitila umboni, Mulungu akuti:

قال تعالى: ( شهد الله أنه لا إله  إلا هو والملائكة وأولو العلم قائما با لقسط لا إ لاه إلا هو العزيز الحكيم )

سزرة العمران : الأية  18           

Mulungu [mwini] akuikila umboni kuti, palibe wopembedzedwa muchoonadi koma iye basi ndipo akuikila umboni [zomwe] Angelo ndi eni nzeru kuti iye ngokhazikitsa chilungamo. Palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma iye. Ngwamphamvu zoposa, ngwa nzeru za kuya.  {Surat Alimran: Ayat 18}

Kumasulira kwa kuyikira umboni kuti ndithu Muhammad ndi mthenga    wa Mulungu;

Ndiko kumutsatira zimene walamula, kumuvomereza zimene wakamba, ndikuzilambalala zimene waletsa ndikukalipa komanso asapembedzedwe Mulungu pokha-pokha kudzera malamulo amene Iye wanena.

Umboni wa Swala, kupereka chopereka ndikumasulira kwa umodzi wa

Mulungu {TAUHID};

Mulungu akuti;

"وما أمروا إلا ليعبدوا الله مخلصين له الدين حنفآء ويقيموا الصلا ة ويؤتوا الزكاة  وذلك دين القيمة."

{سورة البينة الآية 5}

"Sadalamulidwe {china} koma kuti apembedzedwe Mulungu {m`modzi yekha} ndikuyeretsa chipembedzo chake popendekera ku choona {ndikusiya njira zonama} ndikuti asunge Swala ndiponso apereke chopereka {chapa chuma chawo} chimenecho {ndicho} chipembedzo choongoka."

[Surat Bayyina Ayat: 5]

Umboni wosala m`mwezi wa Ramadhan, Mulungu akuti;

"يا أيها الذين ءامنوا كتب عليكم  الصيام كما كتب على الذين من قبلكم لعلكم تتقون."

{سورة البقرة الآية 183}

E! inu amene mwakhulupirira! Kwalamulidwa kwa inu kusala {Ramadhan} monga momwe kudalamulidwa kwa anthu akale, inu musadabwere kuti muope Mulungu {popewa zoletsedwa}.

[Surat Baqara Ayat: 183]

Umboni wa Hajj, Mulungu akuti;

"و لله على الناس حج البيت من استطاع إليه سبيلاً ومن كفر فإن الله غني عن العالمين."

{سورة آل عمران الآية 97}

"Ndipo Mulungu walamula anthu kuti, akachite Hajj kunyumbayo amene angathe kukonzekera ulendo wonka kumeneko. Ndipo yemwe angakane {osapitako pomwe alinazo zomuyenereza} ndithudi Mulungu Ngwa chikwane-kwane pazolengedwa zake."

[Surat Al-Imran Ayat: 97]

GAWO LA CHIWIRI.

CHIKHULUPIRIRO.

Chimenechi chiri ndi nthambi makumi asanu ndi awiri kudzanso mphambu zitatu [73]

Yapamwamba yake ndi; mau onena kuti palibe wina oyenereka kumupembedza mu choonadi koma Mulungu yekha. Yapansi yake, ndi kuchotsa zoyipa mu njira.  Manyazi ndi nthambi imodzi mu nthambi zachikhulupiriro.

 

Tsono nsanamira zachikhulupiriro ziripo zisanu ndi imodzi [6].

Ukhulupilire mwa Mulungu ndi Angelo Ake ndi mabuku Ake ndi atumiki Ake ndi tsiku la chimaliziro komanso muyeso woyikidwa kuchitika zinthu zabwino ndi zoyipa.

Umboni wansanamira zimenezi Mulungu wanena kuti;

"ليس البر أن تولوا وجوهكم قبل المشرق والمغرب ولكن البر من آمن بالله واليوم الآخر والملائكة والكتب والنبيين."

{سورة البقرة الآية 177}

"Ubwino suli potembenuzira nkhope zanu mbali ya kuvuma ndikuzambwe {popemphera Swala} koma ubwino weni-weni ndi {womwe} akukhulupirira Mulungu, tsiku lomaliza, Angelo ndi buku ndi aneneri."

[Surat Baqara Ayat: 177]

Umboni wa muyeso, Mulungu akuti;

"إنا كل شيء خلقناه بقدرٍ ."

{سورة القمر الآية 49}

"Ndithu Ife tachilenga chinthu chiri chonse ndi muyeso {kulingana ndi zolinga}.

[Surat Qamar Ayat: 49]

GAWO LA CHITATU.

UBWINO.

Uli ndi nsanamira imodzi.

Uku ndiko kumugwadira Mulungu ngati ukumuwona, ngakhale sukumuwona koma Mulunguyo akukuwona.

Umboni wake Mulungu wanena kuti;

"إن الله مع الذين اتقوا والذين هم محسنون."

{سورة النحل الآية 128}

"Ndithu Mulungu ali pamodzi ndi amene akumuwopa ndi amenenso akuchita zabwino."

[Surat Nahl Ayat: 128]

Komanso akuti;

"وتوكل على العزيز الرحيم. الذي يراك حين تقوم وتقلبك في الساجدين إنه هو السميع العليم."

{سورة الشعراء الآيات21-22}

"Ndipo tsamira kwa {Mbuye wako} mwini mphamvu zoposa, wachisoni. Yemwe akukuwona pamene ukuyimirira {pamapepmphero} ndikutembenuka tembenuka kwako {pogwetsa mphumi yako pansi ndikudzuka ndikuyimirira} pamodzi ndi ogwetsa mphumi pansi {polambira Mulungu.}

[Surat Shuaraai Ayat: 21-22]

 

Komanso mawu a Mulungu akuti;

"وما تكون في شأن وما تتلوا منه من قرءان ولا تعلمون من عملٍ إلا كنا عليكم شهوداً إن تفيضون فيه."

{سورة يونس الآية 61}

"Ndipo siutanganidwa ndi ntchito ili yonse ndiponso simuwerenga m`menemo {chinthu chiri chonse} cha m`Qurani ndipo simuchita ntchito ina ili yonse {inu anthu} koma Ife timakhala mboni pa inu pamene mukutanganidwa nayo."

[Surat Yunusu Ayat: 61]

Umboni mu zokamba za Mtumiki {SAW} ndi hadith yotchuka ya Jibril;

"عن عمر بن الخطاب رضي الله عنه قال: (بينما نحن جلوس عند النبي صلى الله عليه وسلم إذ طلع علينا رجل شديد بياض الثياب شديد سواد الشعر لا يرى عليه أثر السفر  ولا يعرفه منا أحد. فجلس إلى النبي صلى الله عليه وسلم فأسند ركبتيه إلى ركبتيه ووضع كفيه على فخذيه وقال: يا مدمد أخبرني عن الإسلام فقال: أن تشهد أن لا إله إلا الله وأن محمداً رسول الله وتقيم الصلاة وتؤتى الزكاة وتصوم رمضان وتحج البيت إن استطعت إليه سبيلاً. قال: صدقت. فعجبنا له يسأله ويصدقه. قال: أخبرني عن الإيمان ، قال: أن تؤمن بالله وملائكته وكتبه ورسله واليوم الآخر وبالقدر خيره وشره ، قال: أخبرني عن الإحسان.قال: أن تعبد الله كأنك تراه فإلم تكن تراه فإنه يراك.قال: أخبرني عن الساعةقال: مالمسؤول عنها بأعلم من السائل. قال: أخبرني عن أمارتها. قال : أن تلد الأمة ربتها وأن ترى الحفاة العراة العالة رعاء الشاء يتطاولون في البنيان.قال: فمضى.فلبثنا مليا فقال. يا عمر أتدرون من السائل؟ قلنا: الله ورسوله أعلم .قال. هذا جبريل أتاكم يعلمكم أمر دينكم.)"

Nkhani yachokera kwa Umar Bin L-khataabi {amusangalalile Mulungu iye} anati; Tiri chikhalireni ndi mtumiki {SAW} adatitulukira ife munthu woyera kwambiri zovala zake,tsitsi lake linali lakuda kwambiri, sichinawonekere pathupi pake chisonyezo chiri chonse choti munthuyu anali pa ulendo palibenso aliyense mwa ife anamudziwa. Anakhala pafupi ndi mtumiki SAW nagundanitsa mawondo ake ndi mawondo amtumiki SAW nayikanso manja ake pantchafu za mtumiki SAW nati;

(Iwe Muhammad! Tandiuza za chisilamu. Mtumiki anati;

Uyikire umboni kuti palibe oyenereka kumpembedza mwachoonadi koma Mulungu yekha ndipo Muhammad ndi mthenga wa Mulungu, uyimike Swala, upereke chopereka, usale mwezi wa Ramadhan ndinso uchite Hajj kunyumba ya Mulungu ku Makka ngati uli nazo zokukwaniritsa kuyendera kunka ku maloko.)

Iye anati; wanena zowona.

Tinadabwa naye akufunsa ndikuvomereza kuti wanena zowona.

Kenaka anati; Ndiuze za chikhulupiriro. 

Mtumiki anati;

Ukhulupirire mwa Mulungu ndi Angelo ake ndi mabuku ake ndi atumiki ake ndi tsiku lachimaliziro ndi muyeso oti zabwino ndi zoyipa {zimachokera kwa Mulungu}.

Kenaka anati ndiuze za Ubwino.

Mtumiki anati;

"Umpembedze Mulungu ngati ukumuwona ngakhale suukumuwona koma Iye akukuwona."

Ndipo kenakanso anati;

Ndiwuze za Qiyama {tsiku lachimaliziro};

Mtumiki anati; ofunsidwa zimenezi sali wozindikira kuposa amene akufunsa.

Anatinso, ndiuze za zazisonyezo zake.

Mtumiki anati;

Adzabereka kapolo mbuye wake ndipo udzawona opanda nsapato, amaliseche, osauka, oweta mbuzi akumanga nyumba zapamwamba.

 

Ndipo Umar [RA] anati; Munthu uja anapita. Tidakhala choncho kenako mtumiki adati; Iwe Umar, kodi mukudziwa kuti ndi ndani ofunsa uja? Ife tidati; Mulungu ndi mthenga wake ndi amene akudziwa. Anati; Amene uja ndi Jibril {M`ngelo} anakufikirani kuzakuphunzitsani za chipembedzo chanuchi."

PHATA LACHITATU.

KUMUDZIWA MTUMIKI WANU MUHAMMAD {saw}

Iye ndi Muhammad mwana wa Abdullah mwana wa Abdul-muttalib, mwana wa Hashim, Hashim mwana wa ku mtundu wa Quraish, Quraish ndi wa m`ma Arab, Arab ndi ochokera  muzidzukulu za Ismail mwana wa Ibrahim  mtendere ndi madalitso zikhale kwa Iye.

Adali ndi zaka makumi asanu ndi limodzi ndikudza zaka zitatu. Mzaka zimenezi zaka makumi anayi asadalandire utumiki ndipo zaka makumi awiri ndi zaka zitatu anali pa utumiki ndi uthenga.

 

Adapatsidwa utumiki ndi mawu oti; werenga {إقرأ} ndipo kukhala mthenga ndi mawu woti {مدثر} woziphimba ndi msalu.

Mzinda wake ndi Makka kumene adamtumiza Mulungu pompatsira chenjezo kuti akasiyitse kumphatikiza Mulungu ndi zina, ndikutinso akawayitanire anthu ku umodzi wa Mulungu m`mapemphero {Tauhid}.

 

      Umboni wake Mulungu akuti;

" ياأيها المدثر قم فأنذر.وربك فكبر وثيابك فطهر والرجز فاهجر. ولا تمنن تستكثر ولربك فاصبر."

{سورة المدثر الآيات 1 -7}

"E! Iwe wadziphimba {msalu}. Imirira ndipo uwachenjeze {anthu zachilango cha Mulungu}.  Ndipo mbuye wako {yekha} umkulitse {pomulemekeza}. Ndipo nsalu zako uziyeretse {ndi madzi kuuve}. Ndiponso zoyipa monga mafano ndi zina zonse zipewe. Usapatse anthu ncholinga choti ulandire zambiri. Chifukwa cha Mbuye wako pirira {kumalamulo ake poleka zomwe waletsa ndikuchita zimene walamula}.

[Surat Mudathiru Ayat:1-7]

 

Tanthauzo loti Imirira ndipo uwachenjeze;"

Wachenjeze kuti asiye kumphatikiza Mulungu ndi zina ndipo ayitanire umodzi wake m`mapemphero".

 

Ndipo Mbuye wako umkulitse;

Ndiye kuti umlemekeze pompatsa umodzi wake m`mapemphero".

Ndipo nsalu zako uziyeretse;

Ndiye kuti umlemekeze uyeretse ntchito zako posiya kumphatikiza Iye Mulungu

Ndiponso zoyipa zipewe;

Akutanthauza mafano.

KUPEWA  KWAKE.

Kuwapewa mafanowa ndi eni zimenezi, mkupewanso

Converted with the trial version of Word Cleaner, it will only convert 75% of a document.
To remove this message click here to buy the full version of Word Cleaner now.